Success Stories

Agulupu A Hamid Mtambo ndiokondwa ndi m’gwirizano wa EU ndi mabungwe monga NICE Public Trust Malawi kudzera mu pulogalamu ya Chilungamo

Agulupu A Hamid Mtambo ndiokondwa ndi m’gwirizano wa EU ndi mabungwe monga NICE Public Trust Malawi kudzera mu pulogalamu ya Chilungamo. Pulogamuyi inathandizila kukhazikistidwa kwa liwu la nzika (Citizen Forum) zomwe zalimbikitsa komanso kupatsa mphamvu kwa anthu a muderali. Lero, kudzera mu maphunziro omwe analandira, nzikazi zikugwira bwino ntchito ndi adindo, kulondoloza zinthu zikalakwika komanso kupempha chitukuko kudera lawo. Izi zathandizilia kuveka ufumu a Mfumu yaikulu a Kumtumanji, patapita zaka zambiri opanda mfumu yaikulu ku derali.